Apa ndi pamene ife tiri lero. Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhani yolankhula ndi Mulungu? Za pemphero? Anthu onse, ngakhale amene sakhulupirira Mulungu, angakonde kulankhula naye ngati akanatha. Pali zinthu zitatu zochokera m’Baibulo zimene ndi zabwino kuzidziwa kuti munthu alankhule bwino ndi Mulungu.